Psalms 54

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.”

1Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu;
onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.
2Imvani pemphero langa, Inu Mulungu
mvetserani mawu a pakamwa panga.

3Alendo akundithira nkhondo;
anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga,
anthu amene salabadira za Mulungu.

4Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa;
Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.

5Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe;
mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.

6Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu;
ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova,
pakuti ndi labwino.
7Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse,
ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.
Copyright information for NyaCCL